15 Ayuda onse anayamba kusangalala+ chifukwa cha zimene analumbirazo popeza analumbira ndi mtima wawo wonse, komanso chifukwa chakuti anafunafuna Mulungu mokondwa kwambiri moti iye analola kuti amupeze.+ Choncho Yehova anapitiriza kuwapatsa mpumulo pakati pa adani awo onse owazungulira.+