-
2 Mafumu 11:4Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
4 M’chaka cha 7, Yehoyada+ anatumiza uthenga kwa atsogoleri a magulu a asilikali 100 olondera mfumu Achikariya,+ ndiponso kwa atsogoleri a magulu a asilikali 100 othamanga.+ Anawaitanitsa kuti abwere kwa iye kunyumba ya Yehova ndipo anachita nawo pangano+ n’kuwalumbiritsa+ kunyumba ya Yehova. Kenako anawaonetsa mwana wa mfumu uja.
-
-
1 Mbiri 26:26Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
26 Selomoti ameneyu pamodzi ndi abale ake anali kuyang’anira chuma chonse cha zinthu zimene anaziyeretsa kukhala zopatulika. Amene anayeretsa zinthu zimenezi kukhala zopatulika+ anali Davide+ mfumu, atsogoleri a nyumba za makolo,+ atsogoleri a magulu a anthu 1,000, a magulu a anthu 100, ndi atsogoleri a asilikali.
-