26 Iye anatenga chuma cha m’nyumba ya Yehova ndi chuma cha m’nyumba ya mfumu.+ Anatenga chilichonse+ kuphatikizapo zishango zonse zagolide zimene Solomo anapanga.+
13 Mfumu ya Babulo inatenga chuma chonse cha m’nyumba ya Yehova ndi chuma cha m’nyumba ya mfumu.+ Inaphwanyaphwanyanso ziwiya zonse+ zagolide zimene Solomo mfumu ya Isiraeli anapangira kachisi wa Yehova, monga momwe Yehova ananenera.