13 Ndiyeno ndidzamuimba mlandu+ chifukwa cha masiku amene anapembedza zifaniziro za Baala+ zimene anali kuzifukizira nsembe zautsi.+ Nthawi imeneyi anali kuvala mphete yake ndi zinthu zake zodzikongoletsera.+ Iye anali kutsatira amuna omukonda kwambiri+ ndipo ine anandiiwala,’+ watero Yehova.