-
2 Mbiri 23:18Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
18 Kuwonjezera apo, Yehoyada anapereka ntchito za panyumba ya Yehova kwa ansembe ndi Alevi amene Davide+ anawaika m’magulu panyumba ya Yehova, kuti azipereka nsembe zopsereza za Yehova mogwirizana ndi zimene zinalembedwa m’chilamulo cha Mose.+ Anawauza kuti azizipereka mosangalala poimba nyimbo motsatira ndondomeko imene Davide anakhazikitsa.
-
-
2 Mbiri 31:2Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
2 Kenako Hezekiya anaika magulu+ a ansembe ndi Alevi+ mogwirizana ndi magulu awo. Gulu lililonse analiika mogwirizana ndi utumiki wawo monga ansembe+ ndi Alevi+ ogwira ntchito yokhudza nsembe yopsereza+ ndi nsembe zachiyanjano.+ Anawaika m’maguluwa kuti azitumikira,+ kuyamika+ ndi kutamanda+ Mulungu m’zipata za kachisi wa Yehova.
-