2 Samueli 11:1 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 11 Ndiyeno ku chiyambi kwa chaka,+ pa nthawi imene mafumu anali kupita kukamenya nkhondo,+ Davide anatumiza Yowabu, atumiki ake ndi Isiraeli yense kuti akawononge ana a Amoni+ ndi kuzungulira mzinda wa Raba.+ Koma Davide anatsalira ku Yerusalemu. 1 Mafumu 20:22 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 22 Pambuyo pake mneneri uja+ anapita kwa mfumu ya Isiraeli n’kuiuza kuti: “Pitani, kalimbitseni gulu lanu lankhondo+ ndi kuganizira zomwe mudzachite,+ popeza kumayambiriro kwa chaka chamawa mfumu ya Siriya ija idzabweranso kudzamenyana nanu.”+ 2 Mafumu 13:20 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 20 Pambuyo pa zimenezi Elisa anamwalira ndipo anamuika m’manda.+ Tsopano panali magulu a achifwamba+ achimowabu+ amene ankabwera m’dzikolo kumayambiriro kwa chaka chilichonse.
11 Ndiyeno ku chiyambi kwa chaka,+ pa nthawi imene mafumu anali kupita kukamenya nkhondo,+ Davide anatumiza Yowabu, atumiki ake ndi Isiraeli yense kuti akawononge ana a Amoni+ ndi kuzungulira mzinda wa Raba.+ Koma Davide anatsalira ku Yerusalemu.
22 Pambuyo pake mneneri uja+ anapita kwa mfumu ya Isiraeli n’kuiuza kuti: “Pitani, kalimbitseni gulu lanu lankhondo+ ndi kuganizira zomwe mudzachite,+ popeza kumayambiriro kwa chaka chamawa mfumu ya Siriya ija idzabweranso kudzamenyana nanu.”+
20 Pambuyo pa zimenezi Elisa anamwalira ndipo anamuika m’manda.+ Tsopano panali magulu a achifwamba+ achimowabu+ amene ankabwera m’dzikolo kumayambiriro kwa chaka chilichonse.