27 Akam’mwetsa madziwo, ngati iye anadzidetsa mwa kugona ndi mwamuna wina,+ madzi a tembererowo akalowa m’thupi mwake, azikhala chinthu chowawa. Pamenepo mimba yake izitupa, ndipo ntchafu yake izifota. Mkaziyo azikhala chitsanzo cha wotembereredwa pakati pa anthu amtundu wake.+