22 Zinali choncho chifukwa mfumuyo inali ndi zombo za ku Tarisi+ panyanja pamodzi ndi zombo za Hiramu. Kamodzi pa zaka zitatu zilizonse, zombo za ku Tarisizo zinkabweretsa golide,+ siliva, minyanga ya njovu,+ anyani, ndi mbalame zotchedwa pikoko.
18 Hiramu,+ kudzera mwa antchito ake, ankatumizira Solomo zombo ndi antchito odziwa za panyanja.+ Iwo ankapita ku Ofiri+ pamodzi ndi antchito a Solomo kukatenga golide+ wokwana matalente* 450,+ ndipo anali kubwera naye kwa Mfumu Solomo.+