Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • Genesis 10:4
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 4 Ana a Yavani anali Elisaha,+ Tarisi,+ Kitimu+ ndi Dodanimu.+

  • 2 Mbiri 20:36
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 36 Chotero anayamba kugwira naye limodzi ntchito yopanga zombo zopita ku Tarisi.+ Zombozo anazipangira ku Ezioni-geberi.+

  • Salimo 72:10
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 10 Mafumu a ku Tarisi ndi m’zilumba+

      Adzapereka msonkho.+

      Mafumu a ku Sheba ndi Seba

      Adzapereka mphatso.+

  • Yesaya 23:1
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 23 Uthenga wokhudza Turo:+ Lirani mofuula inu zombo za ku Tarisi,+ chifukwa chakuti mzindawo wasakazidwa ndipo sulinso doko. Sulinso malo oti mungafikepo.+ Anthu amva zimenezi ali kudziko la Kitimu.+

  • Yesaya 60:9
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 9 Pakuti zilumba zidzayembekezera ine.+ Nazonso zombo za ku Tarisi+ zidzayembekezera ine ngati poyamba paja, kuti zikubweretsere ana ako aamuna kuchokera kutali.+ Iwo adzabwera atanyamula siliva ndi golide wawo,+ kuti alemekeze dzina+ la Yehova Mulungu wako ndi Woyera wa Isiraeli,+ pakuti iye adzakhala atakukongoletsa.+

  • Ezekieli 27:12
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 12 “‘“Tarisi+ unali kuchita naye malonda a zinthu zambiri zosiyanasiyana zamtengo wapatali.+ Unamupatsa zinthu zako zimene unasunga posinthanitsa ndi siliva, chitsulo, tini ndi mtovu.+

  • Yona 1:3
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 3 Pamenepo Yona ananyamuka n’kulowera ku Tarisi,+ kuthawa Yehova.+ Kenako anafika ku Yopa+ ndipo kumeneko anapeza chombo chopita ku Tarisi. Iye analipira malipiro a ulendowo n’kukwera chombocho kuti apite ku Tarisi limodzi ndi anthu amene anali m’chombomo, kuthawa Yehova.

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena