7 Choncho anasankha mizinda ina kuti ikhale yopatulika. Mizinda yake inali Kedesi+ ku Galileya m’dera lamapiri la Nafitali, Sekemu+ m’dera lamapiri la Efuraimu, Kiriyati-ariba,+ kutanthauza Heburoni, m’dera lamapiri la Yuda.
24Ndiyeno Yoswa anasonkhanitsa pamodzi mafuko onse a Isiraeli ku Sekemu.+ Iye anaitanitsa akulu a Isiraeli,+ atsogoleri, oweruza, ndi akapitawo, ndipo iwo anaima pamaso pa Mulungu woona.+
9Patapita nthawi, Abimeleki+ mwana wa Yerubaala, anapita ku Sekemu+ kwa abale a mayi ake. Kumeneko anayamba kulankhula nawo ndiponso kulankhula ndi banja lonse la bambo a mayi akewo kuti: