10 Pamenepo Yehova anasokoneza adaniwo pamaso pa Aisiraeli.+ Ndiyeno Aisiraeli anayamba kupha adaniwo kwadzaoneni ku Gibeoni,+ ndi kuwathamangitsa kulowera kuchitunda cha Beti-horoni. Ndipo anapitiriza kuwapha mpaka kukafika ku Azeka+ ndi ku Makeda.+
30 ku Zanowa,+ ku Adulamu+ ndi midzi yake yozungulira, ku Lakisi+ ndi madera ake ozungulira, ku Azeka+ ndi midzi yake yozungulira. Iwo anamanga misasa kuyambira ku Beere-seba mpaka kuchigwa cha Hinomu.+
7 Anamuuza mawu amenewa pamene magulu ankhondo a mfumu ya Babulo anali kumenyana ndi Yerusalemu ndi mizinda ina yonse ya mu Yuda,+ kuphatikizapo Lakisi+ ndi Azeka.+ Mizinda imeneyi inali ndi mipanda yolimba kwambiri+ ndipo ndi imene inali isanawonongedwe pamizinda ya mu Yuda.+