30 Ndipo ndidzafafaniza malo anu opatulika olambirirako+ ndi kugwetsa maguwa anu ofukizirapo zonunkhira. Ndidzaponya mitembo yanu pamwamba pa mafano anu onyansa* opanda moyowo,+ ndipo mudzakhala onyansa kwa ine.+
7 Panali pa nthawi imeneyi pamene Solomo anamangira Kemosi+ malo okwezeka,+ chinthu chonyansa+ cha Mowabu, paphiri+ lomwe linali patsogolo+ pa Yerusalemu. Anamangiranso Moleki malo okwezeka, yemwe ndi chinthu chonyansa cha ana a Amoni.