73 Ndiyeno ansembe,+ Alevi, alonda a pazipata, oimba,+ anthu ena onse pamodzi ndi Anetini+ ndi Isiraeli yense anapita kukakhala m’mizinda yawo.+ Pofika mwezi wa 7+ ana a Isiraeli anali atakhala m’mizinda yawo.+
3 Otsatirawa ndiwo atsogoleri a m’chigawo cha Yuda+ amene anali kukhala m’Yerusalemu,+ koma m’mizinda ya Yuda munali kukhala ansembe,+ Alevi,+ Anetini+ ndi ana a atumiki a Solomo.+ Aliyense wa iwo anali kukhala m’malo ake m’mizinda yawo+ mu Isiraeli.+