7 Bisilamu, Mitiredati, Tabeeli, ndi anzake ena onse analemba kalata kwa Aritasasita mfumu ya Perisiya m’masiku a mfumuyo. Kalatayo anaimasulira m’Chiaramu n’kuilemba m’zilembo za Chiaramu.+
3 Pa nthawi imeneyo Tatenai+ bwanamkubwa wa kutsidya lina la Mtsinje,*+ Setara-bozenai, ndi anzawo anabwera kwa Ayudawo n’kudzawafunsa kuti: “Kodi ndani wakulamulani kuti mumange nyumbayi ndi kumaliza khoma* lamatabwali?”+
6 “Tsopano inu Tatenai+ bwanamkubwa wa kutsidya lina la Mtsinje,*+ Setara-bozenai+ ndi anzanu ndiponso abwanamkubwa aang’ono+ amene ali kutsidya lina la Mtsinje, musakasokoneze kumeneko.+