Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • Deuteronomo 28:49
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 49 “Yehova adzautsa mtundu wakutali, kumalekezero a dziko,+ mtundu umene chilankhulo chake sudzachimva.+ Mtunduwo udzakuukira monga mmene chiwombankhanga chimakhwathulira nyama yake,+

  • Deuteronomo 29:24
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 24 Mitundu yonse idzanena kuti, ‘N’chifukwa chiyani Yehova wachitira dzikoli zimenezi?+ N’chifukwa chiyani mkwiyo wake wayaka kwambiri chonchi?’

  • Deuteronomo 31:17
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 17 Pamenepo mkwiyo wanga udzawayakira tsiku limenelo,+ ndipo ndidzawasiya+ ndi kuwabisira nkhope yanga,+ motero adzakhala chinthu choyenera kuwonongedwa. Masoka ndi zowawa zambiri zidzawagwera,+ ndipo pa tsiku limenelo adzanena kuti, ‘Masoka amenewatu akutigwera chifukwa chakuti Mulungu wathu sali pakati pathu.’+

  • Deuteronomo 32:30
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 30 Kodi munthu mmodzi angathamangitse bwanji anthu 1,000,

      Kapena anthu awiri angapitikitse bwanji anthu 10,000?+

      N’zosatheka, pokhapokha Thanthwe lawo litawagulitsa,+

      Komanso ngati Yehova atawapereka.

  • 1 Mafumu 9:7
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 7 ineyo ndidzachotsa Aisiraeli padziko limene ndawapatsa+ ndipo nyumba imene ndaiyeretsa ndi dzina langa, ndidzaichotsa pamaso panga.+ Aisiraeli adzawapekera mwambi+ ndi kuwatonza pakati pa mitundu yonse ya anthu.

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena