25M’chaka cha 9+ cha ufumu wa Zedekiya, m’mwezi wa 10,+ pa tsiku la 10 la mweziwo, Nebukadinezara+ mfumu ya Babulo anabwera+ ku Yerusalemu pamodzi ndi gulu lake lonse lankhondo. Anabwera kudzachita nkhondo ndi mzindawo ndipo anamanga misasa ndi khoma kuzungulira mzinda wonsewo.+
8 M’mwezi wachisanu, pa tsiku la 7 la mweziwo, kutanthauza m’chaka cha 19+ cha Mfumu Nebukadinezara ya ku Babulo, Nebuzaradani+ mkulu wa asilikali olondera mfumu, mtumiki wa mfumu ya Babulo, anabwera ku Yerusalemu.+
39M’chaka cha 9 cha ulamuliro wa Zedekiya mfumu ya Yuda, m’mwezi wa 10,+ Nebukadirezara mfumu ya Babulo pamodzi ndi gulu lake lonse lankhondo anafika ku Yerusalemu ndi kuzungulira mzindawo.+