7 Ndiyeno m’mwezi woyamba,+ umene ndi mwezi wa Nisani, m’chaka cha 12+ cha Mfumu Ahasiwero, munthu wina anachita Puri+ kapena kuti Maere+ pamaso pa Hamani kuti adziwe tsiku ndi mwezi woyenerera. Choncho Maerewo anagwera mwezi wa 12 umene ndi mwezi wa Adara.+