-
2 Mbiri 33:14Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
14 Pambuyo pa zimenezi, Manase anamanga mpanda kunja+ kwa Mzinda wa Davide,+ kumadzulo kwa Gihoni,+ kuyambira m’chigwa kukafika ku Chipata cha Nsomba.+ Mpandawo unazungulira n’kukafika ku Ofeli+ ndipo unali wautali kwambiri kuchokera pansi kufika pamwamba. Kuwonjezera apo, iye anaika akuluakulu a asilikali m’mizinda yonse ya Yuda yokhala ndi mipanda yolimba kwambiri.+
-