13 Usikuwo ndinatulukira pa Chipata cha Kuchigwa,+ kutsogolo kwa Kasupe wa Chinjoka Chachikulu* ndi kulowera ku Chipata cha Kumilu ya Phulusa.+ Pa nthawiyi, ndinali kuonetsetsa+ mmene mpanda wa Yerusalemu unawonongekera ndiponso mmene moto unawonongera zipata zake.+
39 Anadutsanso pamwamba pa Chipata cha Efuraimu,+ Chipata cha Mzinda Wakale,+ Chipata cha Nsomba+ mpaka kukafika pa Nsanja ya Hananeli,+ Nsanja ya Meya+ ndi ku Chipata cha Nkhosa,+ ndipo anaima pa Chipata cha Alonda.