-
Nehemiya 4:14Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
14 Nditaona kuti akuchita mantha, nthawi yomweyo ndinanyamuka ndi kuuza anthu olemekezeka,+ atsogoleri+ ndi anthu onse kuti: “Musachite nawo mantha+ anthu amenewa. Kumbukirani Yehova, Mulungu wamkulu+ ndi wochititsa mantha.+ Menyerani nkhondo abale anu,+ ana anu aamuna, ana anu aakazi, akazi anu ndi nyumba zanu.”
-
-
Nehemiya 7:5Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
5 Koma Mulungu wanga anaika nzeru mumtima mwanga+ kuti ndisonkhanitse anthu olemekezeka, atsogoleri ndi anthu onse kuti alembetse mayina awo motsatira mzere wawo wobadwira.+ Ndiyeno ndinapeza buku la mndandanda wa mayina a mzere wobadwira+ wa anthu amene anabwera moyambirira kuchokera ku ukapolo. Ndinapeza kuti m’bukumo analembamo izi:
-