28 Iye wandisonyeza kukoma mtima kosatha+ pamaso pa mfumu, pamaso pa aphungu ake,+ ndi pamaso pa akalonga onse amphamvu a mfumu. Ineyo ndinadzilimbitsa chifukwa dzanja+ la Yehova Mulungu wanga linali pa ine, ndipo ndinasonkhanitsa atsogoleri a Aisiraeli kuti apite nane limodzi.