21 Azisamba m’manja ndi mapazi awo kuti asafe.+ Limeneli ndi lamulo kwa iwo mpaka kalekale, likhale lamulo kwa Aroni ndi ana ake ku mibadwo yawo yonse.”+
2 “Uza Aroni ndi ana ake kuti asayandikire zinthu zopatulika za ana a Isiraeli ndi kuipitsa dzina langa loyera.+ Asayandikire zinthu zimene azipatula kuti azipereke nsembe kwa ine.+ Ine ndine Yehova.