-
Esitere 2:3Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
3 Ndiyeno inu mfumu musankhe anthu m’zigawo zonse+ za ufumu wanu. Anthuwo asonkhanitse pamodzi atsikana onse, anamwali okongola, kunyumba ya mfumu yokhala ndi mpanda wolimba kwambiri ya ku Susani,+ m’nyumba ya akazi imene Hegai+ akuyang’anira. Iye ndi munthu wofulidwa wa mfumu+ woyang’anira akazi, amenenso ndi mkulu woyang’anira nyumba ya akazi. Ndipo kumeneko atsikanawo azikawapaka mafuta okongoletsa.
-
-
Esitere 2:12Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
12 Mtsikana aliyense anali kukaonekera kwa Mfumu Ahasiwero pambuyo poti am’chitira zonse zimene amayenera kum’chitira pa miyezi 12 malinga ndi lamulo lokhudza akazi. Atsikanawo anali kuwapaka mafuta a mule*+ miyezi 6 kenako anali kuwapaka mafuta a basamu+ pamodzi ndi mafuta enanso okongoletsa miyezi inanso 6. Akachita zimenezi ndiye kuti amaliza dongosolo lonse lowakongoletsera.
-