Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • Esitere 2:6
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 6 Moredekai anali atatengedwa ku Yerusalemu pamodzi ndi anthu amene anatengedwa kupita ku ukapolo.+ Anthuwa ndi amene anatengedwa pamodzi ndi Yekoniya+ mfumu ya Yuda, amene Nebukadinezara+ mfumu ya Babulo anam’tenga kupita naye ku ukapolo.

  • Esitere 3:8
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 8 Kenako Hamani anauza Mfumu Ahasiwero kuti: “Pali mtundu wina wa anthu umene ukupezeka paliponse+ ndipo ukudzipatula pakati pa anthu m’zigawo zonse za ufumu wanu.+ Malamulo awo ndi osiyana ndi malamulo a anthu ena onse ndipo sakutsatira+ malamulo anu mfumu. Choncho si bwino kuti inu mfumu muwalekerere anthu amenewa.

  • Esitere 7:4
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 4 Pakuti ine ndi anthu a mtundu wanga tagulitsidwa+ kuti tiwonongedwe, tiphedwe ndi kufafanizidwa.+ Ngati tikanagulitsidwa kukhala akapolo aamuna+ ndi akapolo aakazi ndikanakhala chete. Koma musalole kuti tsoka limeneli lichitike chifukwa liwonongetsa zinthu zambiri za mfumu.”

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena