5 Tsopano mwamuna wina, Myuda, anali kunyumba ya mfumu yokhala ndi mpanda wolimba kwambiri ya ku Susani.+ Mwamunayu dzina lake anali Moredekai+ mwana wa Yairi, mwana wa Simeyi amene anali mwana wa Kisi M’benjamini.+
3 Moredekai Myuda anali wachiwiri+ kwa Mfumu Ahasiwero ndipo anali wotchuka pakati pa Ayuda. Khamu lonse la abale ake linali kukondwera naye. Iye anali kuchitira zabwino anthu a mtundu wake ndi kulankhula zamtendere+ kwa ana awo onse.