Genesis 19:3 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 3 Koma Loti anawaumiriza kwambiri+ moti mpaka iwo anapita naye kunyumba kwake. Kumeneko anawakonzera phwando,+ n’kuwaphikira mikate yopanda chofufumitsa,+ ndipo anadya. Oweruza 19:21 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 21 Atatero anatengera Mlevi uja kunyumba kwake+ ndipo anapatsa abulu ake aja chakudya.+ Ndiyeno anasamba mapazi awo+ n’kuyamba kudya ndi kumwa. Mateyu 25:35 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 35 Pakuti ine ndinamva njala koma inu munandipatsa chakudya.+ Ndinamva ludzu koma inu munandipatsa chakumwa. Ndinali mlendo koma inu munandilandira bwino.+ Aheberi 13:2 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 2 Musaiwale kuchereza alendo,+ pakuti potero, ena anachereza angelo mosadziwa.+ 1 Petulo 4:9 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 9 Muzicherezana popanda kudandaula.+
3 Koma Loti anawaumiriza kwambiri+ moti mpaka iwo anapita naye kunyumba kwake. Kumeneko anawakonzera phwando,+ n’kuwaphikira mikate yopanda chofufumitsa,+ ndipo anadya.
21 Atatero anatengera Mlevi uja kunyumba kwake+ ndipo anapatsa abulu ake aja chakudya.+ Ndiyeno anasamba mapazi awo+ n’kuyamba kudya ndi kumwa.
35 Pakuti ine ndinamva njala koma inu munandipatsa chakudya.+ Ndinamva ludzu koma inu munandipatsa chakumwa. Ndinali mlendo koma inu munandilandira bwino.+