Salimo 31:13 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 13 Ndamva zinthu zoipa zimene anthu ambiri akunena,+Ndamva zochititsa mantha kuchokera kumbali zonse.+Akasonkhana pamodzi kundichitira upo,+Amakonza chiwembu kuti achotse moyo wanga.+ Yeremiya 11:19 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 19 Ndipo ine ndinali ngati mwana wa nkhosa wamphongo wokondedwa mwapadera, amene akupita kukaphedwa.+ Ine sindinadziwe kuti andikonzera ziwembu+ ndi kunena kuti: “Tiyeni tiwononge mtengowu pamodzi ndi zipatso zake. Tiyeni timuchotse m’dziko la anthu amoyo,+ kuti dzina lake lisakumbukikenso.” Mateyu 12:24 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 24 Afarisi atamva zimenezi ananena kuti: “Ameneyutu sikuti amatulutsa ziwanda ndi mphamvu zake ayi. Amatero ndi mphamvu ya Belezebule, wolamulira ziwanda.”+ 1 Petulo 2:22 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 22 Iye sanachite tchimo,+ ndipo m’kamwa mwake simunapezeke chinyengo.+
13 Ndamva zinthu zoipa zimene anthu ambiri akunena,+Ndamva zochititsa mantha kuchokera kumbali zonse.+Akasonkhana pamodzi kundichitira upo,+Amakonza chiwembu kuti achotse moyo wanga.+
19 Ndipo ine ndinali ngati mwana wa nkhosa wamphongo wokondedwa mwapadera, amene akupita kukaphedwa.+ Ine sindinadziwe kuti andikonzera ziwembu+ ndi kunena kuti: “Tiyeni tiwononge mtengowu pamodzi ndi zipatso zake. Tiyeni timuchotse m’dziko la anthu amoyo,+ kuti dzina lake lisakumbukikenso.”
24 Afarisi atamva zimenezi ananena kuti: “Ameneyutu sikuti amatulutsa ziwanda ndi mphamvu zake ayi. Amatero ndi mphamvu ya Belezebule, wolamulira ziwanda.”+