Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • Deuteronomo 33:2
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 2 Ndipo anati:

      “Yehova anafika kuchokera ku Sinai,+

      Anathwanima pa iwo kuchokera ku Seiri.+

      Anawala kuchokera kudera lamapiri la Parana,+

      Ndipo anali ndi miyandamiyanda ya oyera ake,+

      Kudzanja lake lamanja kunali ankhondo ake.+

  • 2 Mafumu 6:17
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 17 Kenako Elisa anayamba kupemphera+ kuti: “Inu Yehova, m’tseguleni maso+ chonde kuti aone.” Nthawi yomweyo Yehova anatsegula maso a mtumiki uja, moti anaona kuti dera lonse lamapiri kuzungulira Elisa+ linadzaza ndi mahatchi ndi magaleta ankhondo+ oyaka moto.

  • Danieli 7:10
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 10 Mtsinje wa moto unali kuyenda kuchokera kwa iye.+ Panali atumiki okwana miliyoni imodzi amene anali kumutumikira nthawi zonse,+ ndi atumiki enanso mamiliyoni 100 amene anali kuimirira pamaso pake nthawi zonse.+ Bwalo la milandu+ linakhala pansi, ndipo mabuku anatsegulidwa.

  • Mateyu 26:53
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 53 Kapena ukuganiza kuti sindingapemphe Atate wanga kuti anditumizire magulu ankhondo oposa 12 a angelo nthawi yomwe ino?+

  • Chivumbulutso 5:11
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 11 Kenako, ndinaona ndi kumva mawu a angelo ambiri atazungulira mpando wachifumu limodzi ndi zamoyo zija ndi akulu aja. Chiwerengero chawo chinali miyanda kuchulukitsa ndi miyanda*+ ndiponso masauzande kuchulukitsa ndi masauzande.+

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena