Ekisodo 10:15 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 15 Dzombelo linakuta nthaka yonse ya m’dzikolo+ ndipo dziko linachita mdima.+ Dzombelo linadya zomera zonse za m’dzikolo ndi zipatso zonse za m’mitengo zimene sizinawonongeke ndi matalala,+ moti sipanatsale chobiriwira chilichonse m’mitengo kapena pa zomera m’dziko lonse la Iguputo.+ Salimo 105:34 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 34 Analamula kuti pagwe dzombe,+Ndipo panagwa dzombe losawerengeka la mtundu winawake.+ Amosi 7:1 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 7 Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, anandionetsa masomphenya awa: Ndinamuona akutumiza dzombe, anthu atatsala pang’ono kubzala mbewu zomaliza.+ Nthawi imeneyi inali yobzala mbewu zomaliza, anthu atamweta udzu wopita kwa mfumu.
15 Dzombelo linakuta nthaka yonse ya m’dzikolo+ ndipo dziko linachita mdima.+ Dzombelo linadya zomera zonse za m’dzikolo ndi zipatso zonse za m’mitengo zimene sizinawonongeke ndi matalala,+ moti sipanatsale chobiriwira chilichonse m’mitengo kapena pa zomera m’dziko lonse la Iguputo.+
7 Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, anandionetsa masomphenya awa: Ndinamuona akutumiza dzombe, anthu atatsala pang’ono kubzala mbewu zomaliza.+ Nthawi imeneyi inali yobzala mbewu zomaliza, anthu atamweta udzu wopita kwa mfumu.