Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • Genesis 15:1
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 15 Ndiyeno zimenezi zitachitika, Yehova analankhula ndi Abulamu m’masomphenya,+ kuti: “Usaope+ Abulamu. Ine ndine chishango chako.+ Mphoto yako idzakhala yaikulu kwambiri.”+

  • Deuteronomo 33:29
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 29 Ndiwe wodala Isiraeli iwe!+

      Ndani angafanane ndi iwe,+

      Anthu amene akupulumutsidwa ndi Yehova,+

      Chishango chako chokuthandiza,+

      Amenenso ndi lupanga lako lopambana?+

      Adani ako adzakhala mwamantha chifukwa cha iwe,+

      Ndipo iwe udzayendayenda pamalo awo okwezeka.”+

  • 2 Samueli 22:3
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    •  3 Mulungu wanga ndiye thanthwe langa.+ Ine ndidzathawira kwa iye,

      Iye ndi chishango changa,+ nyanga* yanga+ ya chipulumutso ndi malo anga okwezeka achitetezo.+

      Iye ndi malo anga othawirako,+ Mpulumutsi wanga.+ Mumandipulumutsa ku chiwawa.+

  • Salimo 3:3
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    •  3 Koma inu Yehova ndinu chishango changa,+

      Ulemerero wanga+ ndiponso Wonditukula mutu.+

  • Salimo 84:9
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    •  9 Inu Mulungu chishango chathu, onani,+

      Ndipo yang’anani nkhope ya wodzozedwa wanu.+

  • Salimo 115:9
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    •  9 Iwe Isiraeli, khulupirira Yehova.+

      Iye ndiye thandizo lako ndi chishango chako.+

  • Salimo 119:114
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 114 Inu ndinu malo anga obisalamo ndi chishango changa,+

      Pakuti ndayembekezera mawu anu.+

  • Salimo 144:2
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    •  2 Iye amandisonyeza kukoma mtima kwake kosatha ndipo ndiye malo anga achitetezo,+

      Malo anga okwezeka ndi Wopereka chipulumutso,+

      Chishango+ changa ndi malo anga othawirako.+

      Iye amandigonjetsera mitundu ya anthu.+

  • Miyambo 2:7
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 7 Anthu owongoka mtima, iye amawasungira nzeru zopindulitsa.+ Kwa anthu oyenda ndi mtima wosagawanika, iye amakhala chishango+

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena