Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • Deuteronomo 11:11
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 11 Koma dziko limene mukuwolokerako kuti mukalitenge kukhala lanu ndi dziko lamapiri ndi zigwa.+ Ilo limamwa madzi a mvula, madzi ochokera kumwamba.

  • Yobu 38:37
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 37 Ndani amene ali ndi nzeru zoti angathe kudziwa chiwerengero cholondola cha mitambo,

      Kapena zosungira madzi akumwamba, ndani angathe kuzipendeketsa,+

  • Salimo 147:8
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    •  8 Muimbireni Iye amene amaphimba mapiri ndi mitambo,+

      Amene amakonza mvula kuti igwe padziko lapansi,+

      Amenenso amameretsa udzu wobiriwira m’mapiri.+

  • Yeremiya 10:13
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 13 Mawu ake amapangitsa madzi akumwamba kuchita mkokomo,+ ndipo amachititsa nthunzi kukwera kuchokera kumalekezero a dziko lapansi.+ Iye wapanganso zipata zotulukirapo mvula+ ndipo amatulutsa mphepo yamkuntho m’nkhokwe zake.+

  • Amosi 9:6
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 6 “‘Yehova ndilo dzina+ la amene amamanga makwerero ake kumwamba+ ndi kumanganso nyumba pamwamba pa dziko lapansi limene analikhazikitsa,+ amene amaitana madzi akunyanja+ kuti awakhuthulire panthaka ya dziko lapansi.’+

  • Zekariya 10:1
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 10 “Pemphani Yehova kuti akugwetsereni mvula+ pa nthawi ya mvula yomalizira.+ Pemphani Yehova amene anapanga mitambo yamvula+ ndiponso amene amagwetsera anthu mvula yamphamvu.+ Iye amapereka mbewu m’munda mwa munthu aliyense.+

  • Mateyu 5:45
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 45 kuti musonyeze kuti ndinudi ana a Atate wanu wakumwamba.+ Chifukwa iye amawalitsira dzuwa lake pa anthu oipa ndi abwino, ndi kuvumbitsira mvula anthu olungama ndi osalungama omwe.+

  • Machitidwe 14:17
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 17 Komabe iye sanangokhala wopanda umboni wakuti anachita zabwino.+ Anakupatsani mvula+ kuchokera kumwamba ndi nyengo zimene zokolola zanu zimakhala zambiri. Anadzaza mitima yanu ndi chakudya komanso chimwemwe.”+

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena