Salimo 97:11 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 11 Kuwala kwaunikira wolungama,+Ndipo anthu owongoka mtima akusangalala.+ Yesaya 58:10 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 10 mukapatsa munthu wanjala zinthu zimene inuyo mumakonda,+ ndiponso mukakhutiritsa munthu amene akusautsidwa, kuunika kwanu kudzawala kuti ngwee! mu mdima, ndipo mdima wanu udzakhala ngati masana dzuwa likakhala paliwombo.+ 1 Petulo 2:9 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 9 Koma inu ndinu “fuko losankhidwa mwapadera, ansembe achifumu, mtundu woyera,+ anthu odzakhala chuma chapadera,+ kuti mulengeze makhalidwe abwino kwambiri”+ a amene anakuitanani kuchoka mu mdima kulowa m’kuwala kwake kodabwitsa.+ 1 Yohane 1:5 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 5 Umenewu ndi uthenga umene taumva kuchokera kwa iye ndipo tikuulengeza kwa inu,+ kuti Mulungu ndiye kuwala+ ndipo mwa iye mulibe mdima ngakhale pang’ono.+ Chivumbulutso 22:5 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 5 Komanso, usiku sudzakhalakonso.+ Sadzafunikiranso kuwala kwa nyale kapena kwa dzuwa, chifukwa Yehova Mulungu adzawaunikira.+ Ndipo adzalamulira monga mafumu kwamuyaya.+
10 mukapatsa munthu wanjala zinthu zimene inuyo mumakonda,+ ndiponso mukakhutiritsa munthu amene akusautsidwa, kuunika kwanu kudzawala kuti ngwee! mu mdima, ndipo mdima wanu udzakhala ngati masana dzuwa likakhala paliwombo.+
9 Koma inu ndinu “fuko losankhidwa mwapadera, ansembe achifumu, mtundu woyera,+ anthu odzakhala chuma chapadera,+ kuti mulengeze makhalidwe abwino kwambiri”+ a amene anakuitanani kuchoka mu mdima kulowa m’kuwala kwake kodabwitsa.+
5 Umenewu ndi uthenga umene taumva kuchokera kwa iye ndipo tikuulengeza kwa inu,+ kuti Mulungu ndiye kuwala+ ndipo mwa iye mulibe mdima ngakhale pang’ono.+
5 Komanso, usiku sudzakhalakonso.+ Sadzafunikiranso kuwala kwa nyale kapena kwa dzuwa, chifukwa Yehova Mulungu adzawaunikira.+ Ndipo adzalamulira monga mafumu kwamuyaya.+