1 Samueli 2:10 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 10 Onse olimbana ndi Yehova adzagwidwa ndi mantha.+Motsutsana nawo, iye adzagunda ngati mabingu kumwamba.+Yehova mwiniwake adzaweruza dziko lonse lapansi,+Kuti apereke mphamvu kwa mfumu yake,+Ndi kuti akweze nyanga ya wodzozedwa wake.”+ 1 Samueli 7:10 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 10 Pamene Samueli anali kupereka nsembe yopsereza, Afilisiti anayandikira kuti amenyane ndi Isiraeli. Zitatero, Yehova anachititsa mabingu amphamvu kwambiri+ pa tsiku limenelo kuti asokoneze Afilisiti.+ Choncho Afilisitiwo anagonjetsedwa pamaso pa Isiraeli.+
10 Onse olimbana ndi Yehova adzagwidwa ndi mantha.+Motsutsana nawo, iye adzagunda ngati mabingu kumwamba.+Yehova mwiniwake adzaweruza dziko lonse lapansi,+Kuti apereke mphamvu kwa mfumu yake,+Ndi kuti akweze nyanga ya wodzozedwa wake.”+
10 Pamene Samueli anali kupereka nsembe yopsereza, Afilisiti anayandikira kuti amenyane ndi Isiraeli. Zitatero, Yehova anachititsa mabingu amphamvu kwambiri+ pa tsiku limenelo kuti asokoneze Afilisiti.+ Choncho Afilisitiwo anagonjetsedwa pamaso pa Isiraeli.+