1 Mbiri 5:20 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 20 Pa nkhondoyo iwo anathandizidwa moti Ahagara ndi onse amene anali nawo anaperekedwa m’manja mwawo, popeza anapempha Mulungu kuti awathandize+ ndipo iye anamva kupembedzera kwawo chifukwa anam’khulupirira.+ Salimo 33:21 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 21 Mitima yathu imakondwera mwa iye.+Pakuti timadalira dzina lake loyera.+ Salimo 118:8 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 8 Kuthawira kwa Yehova n’kwabwino+Kusiyana ndi kudalira munthu wochokera kufumbi.+ Miyambo 3:5 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 5 Khulupirira Yehova ndi mtima wako wonse,+ ndipo usadalire luso lako lomvetsa zinthu.+ Yeremiya 17:7 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 7 Wodala ndi munthu aliyense amene amakhulupirira Yehova, amene amadalira Yehova.+
20 Pa nkhondoyo iwo anathandizidwa moti Ahagara ndi onse amene anali nawo anaperekedwa m’manja mwawo, popeza anapempha Mulungu kuti awathandize+ ndipo iye anamva kupembedzera kwawo chifukwa anam’khulupirira.+