Yeremiya 13:17 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 17 Ndipo ngati simudzamvera mawu ake+ ndidzalira ndi kugwetsa misozi m’malo obisika chifukwa cha kunyada kwanu. Maso anga adzatulutsa misozi+ chifukwa chakuti nkhosa+ za Yehova zidzakhala zitagwidwa ndi kutengedwa kupita kudziko lina. Maliro 1:16 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 16 Ndikulirira zinthu zimenezi ngati mkazi.+ Maso anga ine! Maso anga akutuluka misozi.+Pakuti wonditonthoza, munthu woti anditsitsimule, ali kutali ndi ine.Ana anga asiyidwa+ popanda thandizo, pakuti mdani wanga wadzitukumula.+ Danieli 9:3 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 3 Ndinayang’ana+ kwa Yehova Mulungu woona kuti ndimufunefune mwa kupemphera,+ kumuchonderera, kusala kudya, kuvala ziguduli* ndi kudzithira phulusa.+
17 Ndipo ngati simudzamvera mawu ake+ ndidzalira ndi kugwetsa misozi m’malo obisika chifukwa cha kunyada kwanu. Maso anga adzatulutsa misozi+ chifukwa chakuti nkhosa+ za Yehova zidzakhala zitagwidwa ndi kutengedwa kupita kudziko lina.
16 Ndikulirira zinthu zimenezi ngati mkazi.+ Maso anga ine! Maso anga akutuluka misozi.+Pakuti wonditonthoza, munthu woti anditsitsimule, ali kutali ndi ine.Ana anga asiyidwa+ popanda thandizo, pakuti mdani wanga wadzitukumula.+
3 Ndinayang’ana+ kwa Yehova Mulungu woona kuti ndimufunefune mwa kupemphera,+ kumuchonderera, kusala kudya, kuvala ziguduli* ndi kudzithira phulusa.+