Salimo 111:10 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 10 Chiyambi cha nzeru ndicho kuopa Yehova.+ ש [Sin]Onse otsatira malamulo a Mulungu ndi ozindikira.+ ת [Taw]Iye ayenera kutamandidwa mpaka muyaya.+ Miyambo 15:16 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 16 Ndi bwino kukhala ndi zinthu zochepa ukuopa Yehova,+ kusiyana ndi kukhala ndi zinthu zambiri koma uli ndi nkhawa.+ Machitidwe 9:31 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 31 Pamenepo mpingo+ mu Yudeya monse, mu Galileya, ndi mu Samariya unalowa m’nyengo yamtendere, ndipo unakhala wolimba. Popeza kuti unali kuyenda moopa Yehova+ ndiponso kulimbikitsidwa ndi mzimu woyera,+ mpingowo unali kukulirakulira. 2 Akorinto 7:1 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 7 Chotero okondedwanu, popeza talonjezedwa zinthu zimenezi,+ tiyeni tidziyeretse+ ndipo tichotse chinthu chilichonse choipitsa thupi kapena mzimu,+ kwinaku tikukwaniritsa kukhala oyera poopa Mulungu.+ 1 Petulo 1:17 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 17 Ndiponso, ngati mukupempha zinthu kwa Atate, amene amaweruza mopanda tsankho+ malinga ndi ntchito za aliyense, chitani zinthu ndi mantha+ pa nthawi imene muli ngati alendo m’dzikoli.+
10 Chiyambi cha nzeru ndicho kuopa Yehova.+ ש [Sin]Onse otsatira malamulo a Mulungu ndi ozindikira.+ ת [Taw]Iye ayenera kutamandidwa mpaka muyaya.+
16 Ndi bwino kukhala ndi zinthu zochepa ukuopa Yehova,+ kusiyana ndi kukhala ndi zinthu zambiri koma uli ndi nkhawa.+
31 Pamenepo mpingo+ mu Yudeya monse, mu Galileya, ndi mu Samariya unalowa m’nyengo yamtendere, ndipo unakhala wolimba. Popeza kuti unali kuyenda moopa Yehova+ ndiponso kulimbikitsidwa ndi mzimu woyera,+ mpingowo unali kukulirakulira.
7 Chotero okondedwanu, popeza talonjezedwa zinthu zimenezi,+ tiyeni tidziyeretse+ ndipo tichotse chinthu chilichonse choipitsa thupi kapena mzimu,+ kwinaku tikukwaniritsa kukhala oyera poopa Mulungu.+
17 Ndiponso, ngati mukupempha zinthu kwa Atate, amene amaweruza mopanda tsankho+ malinga ndi ntchito za aliyense, chitani zinthu ndi mantha+ pa nthawi imene muli ngati alendo m’dzikoli.+