Salimo 72:2 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 2 Aweruzire anthu milandu mwachilungamo,+Ndipo aweruze milandu ya osautsika ndi ziweruzo zolungama.+ Miyambo 20:28 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 28 Kukoma mtima kosatha ndiponso choonadi zimateteza mfumu,+ ndipo chifukwa cha kukoma mtima kosatha kumeneko mfumu imakhazikitsa mpando wake wachifumu.+ Danieli 4:27 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 27 Chotero inu mfumu, chonde mverani malangizo anga+ ndipo chotsani machimo anu pochita zolungama.+ Muchotsenso zolakwa zanu pochitira chifundo osauka.+ Mukatero, mwina zinthu zidzapitiriza kukuyenderani bwino kwa nthawi yaitali.’”+
28 Kukoma mtima kosatha ndiponso choonadi zimateteza mfumu,+ ndipo chifukwa cha kukoma mtima kosatha kumeneko mfumu imakhazikitsa mpando wake wachifumu.+
27 Chotero inu mfumu, chonde mverani malangizo anga+ ndipo chotsani machimo anu pochita zolungama.+ Muchotsenso zolakwa zanu pochitira chifundo osauka.+ Mukatero, mwina zinthu zidzapitiriza kukuyenderani bwino kwa nthawi yaitali.’”+