Salimo 41:1 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 41 Wodala ndi munthu amene amachita zinthu moganizira munthu wonyozeka.+Pa tsiku la tsoka, Yehova adzamupulumutsa.+ Yesaya 58:7 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 7 Ndimafunanso kuti muzigawira chakudya chanu anthu anjala,+ ndiponso kuti muziitanira m’nyumba zanu anthu osautsika ndi osowa pokhala.+ Ndimafuna kuti mukaona munthu wosavala muzimuveka+ ndiponso kuti musamadzibise kwa abale anu.+ Mika 6:8 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 8 Iwe munthu wochokera kufumbi, iye anakuuza zimene zili zabwino.+ Kodi Yehova akufuna chiyani kwa iwe? Iye akufuna kuti uzichita chilungamo,+ ukhale wokoma mtima+ ndiponso uziyenda modzichepetsa+ ndi Mulungu wako.+ 1 Yohane 3:17 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 17 Koma aliyense amene ali ndi zinthu zofunika pa moyo,+ n’kuona m’bale wake zikumusowa,+ koma osamusonyeza m’bale wakeyo chifundo chachikulu,+ kodi munthu ameneyu amakonda Mulungu?+
41 Wodala ndi munthu amene amachita zinthu moganizira munthu wonyozeka.+Pa tsiku la tsoka, Yehova adzamupulumutsa.+
7 Ndimafunanso kuti muzigawira chakudya chanu anthu anjala,+ ndiponso kuti muziitanira m’nyumba zanu anthu osautsika ndi osowa pokhala.+ Ndimafuna kuti mukaona munthu wosavala muzimuveka+ ndiponso kuti musamadzibise kwa abale anu.+
8 Iwe munthu wochokera kufumbi, iye anakuuza zimene zili zabwino.+ Kodi Yehova akufuna chiyani kwa iwe? Iye akufuna kuti uzichita chilungamo,+ ukhale wokoma mtima+ ndiponso uziyenda modzichepetsa+ ndi Mulungu wako.+
17 Koma aliyense amene ali ndi zinthu zofunika pa moyo,+ n’kuona m’bale wake zikumusowa,+ koma osamusonyeza m’bale wakeyo chifundo chachikulu,+ kodi munthu ameneyu amakonda Mulungu?+