Salimo 26:2 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 2 Ndisanthuleni, inu Yehova, ndi kundiyesa.+Yengani impso zanga ndi mtima wanga.+ Salimo 66:10 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 10 Pakuti inu Mulungu mwatisanthula,+Mwatiyenga ngati siliva.+ Miyambo 21:2 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 2 Njira iliyonse ya munthu imaoneka yowongoka m’maganizo mwake,+ koma Yehova amafufuza mitima.+ Miyambo 24:12 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 12 Ukanena kuti: “Ifetu izi sitinali kuzidziwa,”+ kodi amene amafufuza mitima sazindikira zimenezo?+ Ndipo kodi amene amayang’anitsitsa moyo wako sadziwa zimenezo+ n’kubwezera munthu wochokera kufumbi mogwirizana ndi ntchito yake?+ Yesaya 48:10 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 10 Taonani! Ndinakuyengani koma osati ngati mmene amayengera siliva.+ Ndinakusankhani pamene munali m’ng’anjo ya masautso.+
12 Ukanena kuti: “Ifetu izi sitinali kuzidziwa,”+ kodi amene amafufuza mitima sazindikira zimenezo?+ Ndipo kodi amene amayang’anitsitsa moyo wako sadziwa zimenezo+ n’kubwezera munthu wochokera kufumbi mogwirizana ndi ntchito yake?+
10 Taonani! Ndinakuyengani koma osati ngati mmene amayengera siliva.+ Ndinakusankhani pamene munali m’ng’anjo ya masautso.+