7 Yosefe atawaona abale akewo, anawazindikira nthawi yomweyo, koma anadzisintha kuti asam’dziwe.+ Chotero analankhula nawo mwaukali n’kuwafunsa kuti: “Mwachokera kuti?” Iwo anayankha kuti: “Tachokera kudziko la Kanani, ndipo tabwera kuno kudzagula chakudya.”+