Genesis 29:13 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 13 Tsopano Labani atangomva za Yakobo, mwana wa mlongo wake, anathamanga kukakumana naye.+ Atafika, anam’kumbatira ndi kum’psompsona, n’kupita naye kunyumba kwake.+ Kumeneko, Yakobo anafotokozera Labani zinthu zonse. Genesis 33:4 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 4 Esau anathamanga kudzakumana naye,+ ndipo anamukumbatira+ ndi kum’psompsona. Atakumbatirana, onse awiri anagwetsa misozi kwambiri. Genesis 48:10 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 10 Maso a Isiraeli anali atafooka chifukwa chokalamba,+ moti sankatha kuona. Yosefe anabweretsa anawo pafupi ndi bambo ake, ndipo bambo akewo anawapsompsona anawo n’kuwakumbatira.+ 2 Mafumu 4:16 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 16 Ndiyeno Elisa anati: “Chaka chamawa nthawi ngati yomwe ino mudzakhala mukuyangata mwana wamwamuna.”+ Koma mayiyo atamva anati: “Iyayi mbuyanga, munthu wa Mulungu woona! Musandinamize ine kapolo wanu.”
13 Tsopano Labani atangomva za Yakobo, mwana wa mlongo wake, anathamanga kukakumana naye.+ Atafika, anam’kumbatira ndi kum’psompsona, n’kupita naye kunyumba kwake.+ Kumeneko, Yakobo anafotokozera Labani zinthu zonse.
4 Esau anathamanga kudzakumana naye,+ ndipo anamukumbatira+ ndi kum’psompsona. Atakumbatirana, onse awiri anagwetsa misozi kwambiri.
10 Maso a Isiraeli anali atafooka chifukwa chokalamba,+ moti sankatha kuona. Yosefe anabweretsa anawo pafupi ndi bambo ake, ndipo bambo akewo anawapsompsona anawo n’kuwakumbatira.+
16 Ndiyeno Elisa anati: “Chaka chamawa nthawi ngati yomwe ino mudzakhala mukuyangata mwana wamwamuna.”+ Koma mayiyo atamva anati: “Iyayi mbuyanga, munthu wa Mulungu woona! Musandinamize ine kapolo wanu.”