Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • Deuteronomo 12:18
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 18 Koma udzazidyera pamaso pa Yehova Mulungu wako, pamalo amene Yehova Mulungu wako adzasankhe.+ Udzazidyera pamalowo iweyo, mwana wako wamwamuna, mwana wako wamkazi, kapolo wako wamwamuna, kapolo wako wamkazi ndi Mlevi wokhala mumzinda wanu. Ndipo uzidzasangalala+ pamaso pa Yehova Mulungu wako pa zochita zako zonse.

  • Deuteronomo 20:6
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 6 Kodi pali amene walima munda wa mpesa koma sanayambe kukolola zipatso zake? Achoke ndi kubwerera kunyumba yake, kuopera kuti angafe pankhondo ndipo munthu wina angakolole za m’munda wakewo.+

  • Mlaliki 3:22
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 22 Ine ndaona kuti palibe chabwino kuposa kuti munthu asangalale ndi ntchito yake,+ pakuti imeneyo ndi mphoto yake, popeza palibe amene adzam’bweretse kuti adzaone zimene zizidzachitika iye atafa.+

  • Mlaliki 5:18
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 18 Chinthu chabwino kwambiri ndiponso chokongola chimene ine ndaona, n’chakuti munthu ayenera kudya, kumwa ndi kusangalala, chifukwa cha ntchito yake yonse yovuta+ imene amaigwira mwakhama padziko lapansi pano, kwa masiku onse a moyo wake amene Mulungu woona wam’patsa. Pakuti imeneyo ndiyo mphoto yake.

  • Mlaliki 8:15
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 15 Ineyo ndinatamanda kusangalala,+ chifukwa palibe chabwino chimene anthu angachite padziko lapansi pano kuposa kudya, kumwa ndi kusangalala, pamene akugwira ntchito mwakhama masiku onse a moyo wawo,+ amene Mulungu woona wawapatsa padziko lapansi pano.+

  • Machitidwe 14:17
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 17 Komabe iye sanangokhala wopanda umboni wakuti anachita zabwino.+ Anakupatsani mvula+ kuchokera kumwamba ndi nyengo zimene zokolola zanu zimakhala zambiri. Anadzaza mitima yanu ndi chakudya komanso chimwemwe.”+

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena