12 Pa zikondwerero zawo amaimbapo azeze, zoimbira za zingwe, maseche, ndi zitoliro ndipo amamwapo vinyo.+ Koma sayang’ana ntchito ya Yehova, ndipo ntchito ya manja ake saiona.+
7 Anthu anga atsimikiza kuti akhale osakhulupirika kwa ine.+ Akuwaitana kuti abwerere kwa amene ali wokwezeka, koma palibe ngakhale ndi mmodzi yemwe amene akuimirira.