Genesis 7:16 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 16 Zimene zinali kulowazo, zazimuna ndi zazikazi zamtundu uliwonse, zinalowa monga mmene Yehova anamulamulira Nowa. Kenako Yehova anatseka chitseko.+ Ekisodo 12:22 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 22 Mukatero mutenge kamtengo ka hisope+ n’kukaviika m’beseni la magazi ndi kuwaza pafelemu la pamwamba pa chitseko, ndipo ena mwa magaziwo muwaze pamafelemu awiri a m’mbali mwa khomo. Aliyense asatuluke m’nyumba yake mpaka m’mawa. Salimo 32:7 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 7 Ndinu malo anga obisalamo, mudzanditeteza ku masautso.+Mudzachititsa kuti chisangalalo chindizungulire pamene mukundipulumutsa.+ [Seʹlah.] Salimo 91:4 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 4 Adzakutchinjiriza ndi mapiko ake,+Udzathawira pansi pa mapiko ake.+Choonadi chake+ chidzakhala chishango chako+ chachikulu ndi malo ako achitetezo. Miyambo 18:10 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 10 Dzina la Yehova ndi nsanja yolimba.+ Wolungama amathawira mmenemo ndipo amatetezedwa.+
16 Zimene zinali kulowazo, zazimuna ndi zazikazi zamtundu uliwonse, zinalowa monga mmene Yehova anamulamulira Nowa. Kenako Yehova anatseka chitseko.+
22 Mukatero mutenge kamtengo ka hisope+ n’kukaviika m’beseni la magazi ndi kuwaza pafelemu la pamwamba pa chitseko, ndipo ena mwa magaziwo muwaze pamafelemu awiri a m’mbali mwa khomo. Aliyense asatuluke m’nyumba yake mpaka m’mawa.
7 Ndinu malo anga obisalamo, mudzanditeteza ku masautso.+Mudzachititsa kuti chisangalalo chindizungulire pamene mukundipulumutsa.+ [Seʹlah.]
4 Adzakutchinjiriza ndi mapiko ake,+Udzathawira pansi pa mapiko ake.+Choonadi chake+ chidzakhala chishango chako+ chachikulu ndi malo ako achitetezo.