-
Yesaya 9:7Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
7 Ulamuliro wake wangati wa kalonga udzafika kutali+ ndipo mtendere sudzatha+ pampando wachifumu wa Davide+ ndiponso mu ufumu wake, kuti iye achititse ufumuwo kukhazikika+ ndi kukhala wolimba pogwiritsa ntchito chilungamo,+ ndiponso pogwiritsa ntchito mtima wowongoka,+ kuyambira panopa mpaka kalekale.* Yehova wa makamu adzachita zimenezi modzipereka kwambiri.+
-
-
Zekariya 9:9Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
9 “Iwe mwana wamkazi wa Ziyoni sangalala kwambiri.+ Fuula mokondwera+ iwe mwana wamkazi wa Yerusalemu. Taona, mfumu yako+ ikubwera kwa iwe.+ Mfumuyo ndi yolungama ndipo yapambana.+ Iyo ndi yodzichepetsa+ ndipo ikubwera itakwera bulu. Ikubwera itakwera nyama yokhwima, imene ndi mwana wamphongo wa bulu.+
-