Salimo 2:6 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 6 Ndipo adzanena kuti: “Inetu ndakhazika mfumu yanga+Pa Ziyoni,+ phiri langa lopatulika.”+ Yesaya 32:1 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 32 Taonani! Mfumu+ idzalamulira mwachilungamo,+ ndipo akalonga+ adzalamuliranso mwachilungamo. Yeremiya 23:5 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 5 “Taonani! Masiku adzafika,” watero Yehova, “ndipo Davide ndidzamuutsira mphukira yolungama.+ Ndithudi mfumu idzalamulira+ m’dzikoli ndi kuchita zinthu mozindikira, motsatira malamulo komanso mwachilungamo.+ Luka 19:38 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 38 Iwo anali kunena kuti: “Wodalitsidwa Iye wobwera monga Mfumu m’dzina la Yehova!+ Mtendere kumwamba, ndi ulemerero kumwambamwambako!”+ Yohane 1:49 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 49 Natanayeli anamuyankha kuti: “Rabi, ndinudi Mwana wa Mulungu,+ ndinu Mfumu+ ya Isiraeli.”
5 “Taonani! Masiku adzafika,” watero Yehova, “ndipo Davide ndidzamuutsira mphukira yolungama.+ Ndithudi mfumu idzalamulira+ m’dzikoli ndi kuchita zinthu mozindikira, motsatira malamulo komanso mwachilungamo.+
38 Iwo anali kunena kuti: “Wodalitsidwa Iye wobwera monga Mfumu m’dzina la Yehova!+ Mtendere kumwamba, ndi ulemerero kumwambamwambako!”+