Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • Yesaya 60:18
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 18 “M’dziko lako simudzamvekanso zachiwawa. Mkati mwa malire ako simudzakhalanso kusakaza kapena kuwononga.+ Mipanda yako udzaitcha Chipulumutso+ ndipo zipata zako udzazitcha Chitamando.

  • Yesaya 65:22
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 22 Sadzamanga wina n’kukhalamo. Sadzabzala wina n’kudya. Pakuti masiku a anthu anga adzakhala ngati masiku a mtengo,+ ndipo anthu anga osankhidwa mwapadera adzapindula mokwanira ndi ntchito ya manja awo.+

  • Yeremiya 23:6
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 6 M’masiku a mfumu imeneyi, Yuda adzapulumutsidwa,+ ndipo Isiraeli adzakhala mwabata.+ Dzina la mfumuyi lidzakhala Yehova Ndiye Chilungamo Chathu.”+

  • Ezekieli 34:25
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 25 “‘“Ine ndidzachita nazo pangano la mtendere.+ Ndidzachotsa zilombo zolusa zakutchire m’dzikomo.+ Nkhosazo zidzakhala m’chipululu popanda choziopsa ndipo zizidzagona m’nkhalango.+

  • Hoseya 2:18
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 18 Pa tsiku limenelo ndidzachita pangano ndi chilombo chakuthengo,+ cholengedwa chouluka m’mlengalenga ndi cholengedwa chokwawa panthaka, kuti ndithandize anthu anga. Ndidzathyola uta ndi lupanga ndipo ndidzathetsa nkhondo padziko.+ Pamenepo ndidzawachititsa kukhala mwabata.+

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena