17 “Ansembe ndi atumiki a Yehova alire m’khonde mwa guwa lansembe+ ndipo anene kuti, ‘Inu Yehova, mverani chisoni anthu anu ndipo musachititse manyazi cholowa chanu+ kuti mitundu ya anthu iwalamulire. Anthu a mitundu ina asanene kuti: “Kodi Mulungu wawo ali kuti?”’+