20 “M’masiku amenewo ndiponso pa nthawi imeneyo,+ cholakwa cha Isiraeli chidzafufuzidwa+ koma sichidzapezeka,” watero Yehova. “Machimo a Yuda+ adzafufuzidwa koma sadzapezeka, pakuti ine ndidzakhululukira anthu amene ndawasiya amoyo.”+
9 Koma ine ndinachita zinthu molemekeza dzina langa kuti lisadetsedwe pamaso pa anthu a mitundu ina amene iwo anali kukhala pakati pawo,+ pakuti ndinawachititsa kuti andidziwe pamaso pa anthu a mitundu inawo powatulutsa m’dziko la Iguputo.+