34 Mpaka lero akutsatirabe zipembedzo zawo zakale.+ Palibe amene ankaopa Yehova+ ndipo palibe amene ankatsatira malamulo ake, zigamulo zake,+ ndi chilamulo+ chimene Yehova analamula ana a Yakobo.+ Yakoboyo Mulungu anamusintha dzina n’kumutcha Isiraeli,+